1 minute read

Chichewa

MADZI

Olemba: Owen Khwerusa

Advertisement

“Pali mfundo zingapo zomwe zimayenera kutsatidwa pamene tikumwa madzi

Malamulo angapo amayendetsa thanzi kuti likhale la thanzi kwa nthawi yaitali. Mwachidule malamulo onse amatchulidwa kuti NEWSTART pachingerezi. Kumwa madzi ndi limodzi mwa malamulowa. Pali mfundo zingapo zomwe zimayenera kutsatidwa pamene tikumwa madzi. Gawo lino tikambako zina mwa mfundo zimenezi. • Imwani madzi osachepera 2 litres tsiku ndi tsiku. • Mukangodzuka m’mawa imwani matambula awiri a madzi musanadye kali konse. Izi zimabwezeretsa Vitamin B12 m’thupi mwanu amene amasungidwa mkamwa m’mawa uliwonse. Tikhoza kuika juwisi wa mandimu, molasses kapena uchi. • Osamwa madzi ndi kudya chakudya nthawi imodzi • Mukatha kudya dikirani ma ola 2 musanamwe madzi • Ngati mwamwa madzi dikirani mphindi 30 musanadye chakudya • Sambani madzi otentha kapena ozizira tsiku ndi tsiku. Ngati mumadwala diabetes (nthenda ya shuga) musasambe madzi otentha. MADZI A MOYO

Madzi ndi ofunika ku moyo, ndipo Khristu akuwagwiritsa ntchito ngati fanizo la chipulumutso. Atati mulungu aletse madzi pa dziko la pansi, ingakhale kwa nthawi pang’ono, ndipo ndi m’khalidwe wosautsa wotani ungatsatire. Kulira koposa kwa tsoka losaneneka kungachokere kwa osautsika okhalamo (m’dziko). Ndi kutsatira kwakukulu kwanji kungadze, ngati kuwala kwa choonadi, komwe kuli kofunika ku thanzi ndi umoyo wa moyo wa munthu, kutachotsedwa! Ambiri mu dziko la infali ali kutayika kufuna madzi a moyo. Kutayika kwa moyo uno ndi kosakhala kwa tsoka, koma kutaya moyo omwe uli wa muyaya, omwe muyeso wake ulingana ndi moyo wa mulungu, komwe kuli koopsa kukuganizira; kumeneku ndi kutayika kwa muyaya. Nanga ndi chifukwa ninji pali kuchuluka mphwayi? Chifukwa ninji iwo okhala ndi chidziwitso cha Yesu Khristu akungokhala mwachibwana? Mrs E. G. White mu The Review and Herald Jan 8, 1889 (Leah Zuze womasulira)

This article is from: