2 minute read

Chichewa

Next Article
Chichewa

Chichewa

KUSAMALIRA

MANO By Owen Khwerusa

Advertisement

Mukatha kudya tsukani mkamwa nthawi zonse.” Awa ndi mawu omwe timauzidwa posamalira mano kuti tipewe matenda a mano, fungo loipa komanso pofuna kuoneka bwino poyankhula. Pali mfundo zingapo zomwe timayenera kutsatira pamene tikusamalira mano. • Tsukani mkamwa pang’onopang’ono ndinso mosamala mukangotha kudya. Tsukani mkamwa kawiri patsiku; tikatha kudya kadzutsa komanso madzulo tisanapite kukagona kapena tikangotha kudya mgonero. • Tsukani mbali ya mkati ya mano anu m’mene mwaundana zosalira za zakudya. Tsukani angakhale zosalirazo sizikuoneka. • Dutsitsani mswachi moyandikana ndi nkhama za mano anu. • Tsukani mbali yakunja ya mano anu. Pititsani mswachi cham’mbuyo ndinso mtsogolo. • Ikani mswachi ndikuika pamwamba pa mano anu. Pititsani mswachi wanu mozungulitsa pamwamba pa mano. • Tsukani m’mipata mwa mano anu pogwiritsa ntchito zotokotsera m’mano (dental floss) kapena ulusi. • Tokosani kamodzi patsiku kuti muchotse zotsalira m’mipata mwa mano zisanayambitse matenda m’khama. • Sinthani mswachi wanu pakatha miyezi itatu.

Mswachi wabwino ukuyenera kufikira mbali zonse za mano ndipo mitu yake ikuyenera kukhala yofewa. Mitu yolimba imakanda mano ndipo amaonongeka mwansanga. • Gwiritsani ntchito makala, molasses, juwisi wa mandimu kapena mchere potsuka mkamwa nthawi zonse. Kuphatikidza makala, molasses ndi mchere zimathandizanso kwambiri. “ Gwiritsani ntchito makala, • Pewani kugwiritsa ntchito mankhwala molasses, juwisi wa mandimu otsukira mano okhala ndi flukapena mchere potsuka mkamwa nthawi zonse... oride ochuluka popeza amaononga mawaya a ubongo[1]. • Osamwa kapena kudya zakudya zimene zimakhala ndi caffeine kapena nicotine monga cocacola, masamba a tea, coffee ndi chocolate. Izi zimaononga mano ndipo zimayambitsa fungo loipa mkamwa. • Musadye kapena kumwa zakudya zowotcha kapena zozizira kwambiri poti zimaononga mano; chotero pewani ice cream, madzi a mu

fridge ndi zakumwa zoziziritsa kukhosi. • Musagwiritse ntchito zotokokosela zolimba (tooth picks). Zimanonga mkhama ndi mano. • Mukadya chakudya wonetsetsani kuti padutse ma ola asanu musanadyenso chakudya china. Chifu komanso mano zimafunika kupuma. Mukhoza kumamwa madzi nthawi iliyonse kupatula pokudya. • Pewani kumwa mankhwala achipatala aliwonse mwachisawawa pamene dzino lawawa chifukwa chobooka. • Idyani zipatso, masamba, zakudya zosakonola, mbewu ndi mitedza. Idyani mwakasinthasintha. • Mupewe zothira shuga chifukwa shuga amasokoneza chitetezo cha m’thupi komanso amaoletsa mano. • Mukadya zipatso zokhala ndi asidi monga mandimu, malalanje ndi zina zonga izi, dikirani kwa ola limodzi musanatsuke mkamwa. Asidi amafewetsa mano. • Uchi kapena zotsekemeretsa zina zikhoza kugwiritsidwa ntchito mmalo mwa shuga, koma angakhale izi, ziyenera kukhala zochepa patsiku. Miyambo 24:13 “Mwananga idya uci pakuti ngwabwino…” Miyambo 25:27 “Kudya uci wambiri sikuli kwabwino.” Kupewa kuposa kuchidza. Samalani mano anu! 1. mutha kuwerenga pa: (https://doi. org/10.1016/S2173-5808(11)70062-1

This article is from: